THE INTERNATIONAL BILL OF HUMAN RIGHTS With Multilingual UDHR

 
 
International Covenant on Civil and Political Rights | International Covenant on Economic Social and Cultural Rights
 
   

 

 

 

 

 

 

FL

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

CHECHEWA ( Nyanja ) LANGUAGE

 

Native to : ZAMBIA | MALAWI | MOZAMBIQUE | MALAWI

 

Click on The BLUE Panel To Open or Close The UDHR

CHECHEWA ( Nyanja ) Universal Declaration Of Human Rights

Usage By Country
Officially Recognized Language: Malawi 

Official language in
 Malawi
 Zimbabwe
Native Name Nyanja 


 
Native speakers
12 million  (2007)

 

Total Speakers 10.000.000 (1994) 

LANGUAGE CODES

ISO 639-1 ny
ISO 639-2 nya
ISO 639-3 nya

 

 

 
Recognised minority language in
 Zambia

 

Background 
Spoken by the Chewa and Nyanja people. There are 3,200,000 speakers in Malawi, 989,000 in Zambia and 423,000 in Mozambique with a few in Tanzania. It belongs to the Niger-Congo, Atlantic-Congo, Volta-Congo, Benue-Congo, Bantoid family. 

 

 

CHECHEWA Universal Declaration Of Human Rights

 

Chikalata Cha Mgwirizano Chofotokoza Za Ufulu Wa Chibadwidwe Wa Munthu Aliyense

Chidavomerezedwa ndi kulengezedwa ndi msonkhano waukulu mu mfundo 217A (III) ya pa 10th December, 1948.

Mau Otsogolera

Popeza kuzindikira kuti kudzilemekeza ndi kufanana kwa anthu pa chibadwidwe ndiwo maziko aufulu, chilungamo ndi mtendere pa dziko lapansi,

Popeza kusalabadira ndi kunyoza ufulu wa munthu kwachititsa mchitidwe wa nkhaza womwe wakhumudwitsa chikumbumtima cha anthu, ndipo kukhazikitsa kwa dziko m'mene anthu adzasangalale ndi kulankhula za kukhosi ndiponso kukhulupilira mopanda mantha ndi kusowa kwalengezedwa ngati chinthu cha mtengo wapatali chimene anthu wamba amalakalaka.

Popeza nkofunikira ngati munthu saumilizidwa kutero, ngati chinthu chamapeto, kugaukira ulamuliro wankhanza ndi kuponderezedwa, kuti ufulu wa munthu utetezedwe ndi malamulo,

Popeza nkofunikira kupititsa mtsogolo ubale wa pakati pa maiko,

Popeza anthu a mu bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations) m'chikalata chawo  (Charter of United Nations) anatsikimikizira chikhulupiliro chawo mu ufulu wa munthu ndi kusasiyanitsa pakati pa mwamuna ndi mkazi ndiponso atsimikiza kupititsa mtsogolo chikhalidwe cha anthu ndi umoyo wao,

Popeza maiko mgwirizano alonjeza kukwaniritsa mogwirizana ndi bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations) kupititsa mtsogolo kulemekeza ndi kutsatira malamulo a ufulu wa munthu,

Popeza kumvetsetsa ufulu umenewu nkofunika kwambiri kuti lonjezo limeneli likwaniritsidwe,

Choncho, tsopano,

Msonkhano, Waukulu,

ukulengeza malamulo omwe ali m'chikalata cha mgwirizano chofotokoza za ufulu wa chibadwidwe wa munthu aliyense ngati muyeso wa chikwaniritso kwa anthu onse ndi maiko onse, pachifukwa ichi aliyense ndi bungwe lililonse m'dziko, poganizira za chikalatchi, lidzayesetsa pophunzitsa, maphunziro ndi njira zina zotsogola kupititsa mtsogolo kulemekeza ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina m'dziko kudzanso pakati pa maiko, poonetsetsa kuti mfundozi zikuzindikiridwa ndiponso kutsatidwa pakati pa anthu ndi maiko a mu mgwirizano ndi anthu a m'madera amene maikowo akulamulira.

Ndime 1

Anthu onse amabadwa aufulu ndiponso ofanana mu ulemu ndi ufulu wao.  Iwowa ndi wodalitsidwa ndi mphamvu zoganiza ndi chikumbumtima ndipo achitirane wina ndi mnzake mwaubale.

Ndime 2

Aliyense ali ndi ufulu wa chibadwidwe ndi ufulu wina omwe walembedwa m'chikalata chino, mosasiyanitsa m'mjira iliyonse monga mtundu, maonekedwe a khungu, mwamuna kapena mkazi, chiyankhulo, chipembedzo, ndale kapena maganizo ena, dziko lochokera kapena chikhalidwe, katundu ndi chuma, kubadwa kapena m'mene munthu alili.

Poonjezerapo pasakhale kusiyanitsa poganizira ndale, malamulo kapena m'mene dziko kapena dera lomwe munthu akuchokera lilili, kaya ndi loima palokha, lodalira ena, losadzidalira, kapena lomwe likupingidwa m'njira zina.

Ndime 3

Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi moyo, mtendere ndi chitetezo chathupi.

Ndime 4

Palibe munthu amene adzasungidwe mu ukapolo kapena mwaukapolo; ukapolo ndi malonda a akapolo adzathetsedwa m'njira zonse.

Ndime 5

Palibe amene adzachitiridwe nkhaza kapena kuzunzidwa kapena kupatsidwa chilango monyozedwa.

Ndime 6

Aliyense ali ndi ufulu kuzindikiridwa ngati munthu kulikonse pamaso pa lumulo.

Ndime 7

Aliyense ndi ofanana pamaso pa lamulo ndipo ali oyenera kutetezedwa mosasiyanitsa ndi lamulo.  Aliyense ali oyenera kutetezedwa ku tsankho la mtundu uliwonse lomwe likututsa chikalata chino kudzanso kuyambitsa tsankho lililonse la mtundu wotere.

Ndime 8

Aliyense ali ndi ufulu wolandira chithanzizo chokwanira ndi bwalo la milandu lodalirika pa zochita zophwanya ufulu wa munthu womwe waperekedwa kwa iye ndi malamulo a dziko.

Ndime 9

Palibe amene adzamangidwe, kusungidwa osazengedwa mlandu kapena kuumirizidwa kuchoka m'dziko lake mosatsatira lamulo.

Ndime 10

Aliyense ali ndi ufulu womveredwa mosasiyanitsa ndi bwalo la milandu loyima palokha ndipo losakondera, poganizira ufulu wa munthu ndi udindo wake ndiponso mlandu uliwonse womukhudza.

Ndime 11

 1. Aliyense wozengedwa mlandu asaganiziridwe kuti ndi wolankwira lamulo ndipo asam'zenge mlandu potsatira malamulo ena amene ali ovomerezeka m'dzikomo kapena pakati pa maiko, koma omwe pa nthawi yolakwirayo sanali ovomerezeka.

 2. Chimodzimodzinso chilango chokhwima kuposa chomwe chidalipo panthawi yolakwira lamuloyo chisaperekedwe.

Ndime 12

Palibe amene adzasokonezedwe chinsinsi chake, banja lake, kwawo, kapena makalata ake, kapena zochitika zina zoyenera pa ulemu ndi mbiri yake.  Aliyense ali ndi ufulu kutetezedwa ndi lamulo ngati zoterezi zichitika.

Ndime 13

 1. Aliyense ali ndi ufulu kuyenda ndi kukhala m'kati mwamalire a dziko lililonse.

 2. Aliyense ali ndi ufulu kuchoka m'dziko lililonse kuonjezerapo lake, ndiponso kubwerera ku dziko lake.

Ndime 14

 1. Aliyense ali ndi ufulu kupeza mpumulo ndi kusangalala m'maiko ena m'mene angatetezedwe ku nkhaza.

 2. Ufuluwu sungagwiritsidwe ntchito pa mlandu umene sukukhudza ndale, kapena mchitidwe omwe sugwirizana ndi zolinga ndi mfundo za bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations).

Ndime 15

 1. Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi mtundu.

 2. Palibe amene adzalandidwe mtundu wake kapena kuletsedwa kusintha mtundu wake mosatsatira malamulo.

Ndime 16

 1. Amuna ndi akazi okhwima m'maganizo ndi mu msinkhu, mosaganizira mtundu, maonkedwe a khungu kapena chipembedzo, ali ndi ufulu kukwatira kapena kukwatiwa ndi kuyamba banja.  Iwowa ali ndi ufulu, ofanana pankhani za ukwati, pomwe ali mbanja kudzanso pothetsa banja.

 2. Ukwati udzamangidwa pokhapokha ngati anthu ofuna kumanga banjawo avomereza mosakakamizidwa.

 3. Banja ndi lofunika kwambiri pachikhalidwe cha anthu choncho n'kofunika kuti lipatsidwe chitetezo ndi dziko.

Ndime 17

 1. Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi katundu kapena chuma payekha kapena mogwirizana ndi ena.

 2. Palibe amene adzalandidwa katundu kapena chuma mosatsatira malamulo.

Ndime 18

Aliyense ali ndi ufulu wamaganizo, chikumbumtima ndi chipembedzo; ufuluwu ukhudzanso ufulu wotha kusintha chipembedzo kapena chikhulupiliro, ndi mtendere, kaya payekha kapena mogwirizana ndi ena, pagulu kapena mwachinsinsi, kuonetsa chipembedzo kapena chikhulupiliro pophunzitsa, kuchita, kupembedza ndi kutsatira chipembedzocho.

Ndime 19

Aliyense ali ndi ufulu kuganiza ndi kulankhula, zakukhosi, ufuluwu ukukhudzanso kukhala ndi maganizo popanda chopinga ndiponso kufufuza, kulandira ndi kufalitsa mauthenga ndi maganizo a mtundu uliwonse kudzera pa wailesi kapena njira ina iliyonse popanda malire.

Ndime 20

 1. Aliyense ali ndi ufulu kulowa bungwe lililonse ndi kusonkhana mwamtendere.

 2. Pasakhale munthu aliyense amene angakakamizidwe kulowa bungwe lililonse.

Ndime 21

 1. Aliyense ali ndi ufulu kutenga nawo mbali pa kayendetsedwe ka dziko lake, mwa iye mwini kapena kudzera mwa nthumwi yosankhidwa mosaumirizidwa.

 2. Aliyense ali ndi ufulu wofanana pofuna ntchito zoyendetsedwa ndi boma m'dziko lake.

 3. Chifuniro cha anthu ndicho chikhale magwero a mphamvu za boma; chifunirochi chidzaonetsedwa pochita chisankho choona kawirikawiri chomwe chidzakhale cha aliyense ndiponso chosakondera, ndipo chidzakhala cha chinsinsi kapena cha njira ina iliyonse yofanana ndi iyi.

Ndime 22

Aliyense, monga m'modzi wa gulu la anthu, ali ndi ufulu kulandira chithandizo kuchokera ku boma ndipo adzakwaniritsa izi, kudzera m'mphamvu za dziko, ndi mgwirizano ndi maiko ena ndiponso motsatira kayendetsedwe ndi kapezedwe ka chuma ka dziko lililonse, chithandizo cha chuma, zofunikira pa moyo ndi chikhalidwe chake zomwe ndi mbali ya ulemu wake ndipo n'zofunika pa kakulidwe ka umunthu wake.

Ndime 23

 1. Aliyense ali ndi ufulu kugwira ntchito, kusankha ntchito yomwe akufuna, kukhala ndi zoyenereza pa ntchito, ndiponso kutetezedwa ku ulova.

 2. Aliyense, mopanda tsankho, ali ndi ufulu kulandira malipiro ofanana pa ntchito yofanana.

 3. Aliyense amene akugwira ntchito ali ndi ufulu kulandira malipiro oyenera otha kumupatsa iye ndi banja lake moyo wodzilemekeza ndiponso, ngati n'kofunika, apeze njira zina zodzitetezera pa umoyo wake.

 4. Aliyense ali ndi ufulu kukhazikitsa kapena kulowa mabungwe a anthu ogwira ntchito pofuna kuteteza zomupindulira zake.

Ndime 24

Aliyense ali ndi ufulu kupuma ndi kupeza msangulutso kuonjezerapo kukhala ndi maola ogwilira ntchito oyenera ndiponso tchuthi cholipilidwa nthawi ndi nthawi.

Ndime 25

 1. Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi moyo wathanzi payekha kapena ndi banja lake, kuonjezerapo kukhala ndi chakudya, zovala, nyumba ndi chithandizo cha mankhwala ndi zina zofunikla pa umunthu wake, ndiponso ufulu wa chitetezo ngati iye sali pa ntchito, akudwala, walumala, wafedwa, wakalamba, kapena akusowa zofunika pa moyo wake pa zifukwa zimene iye sangathe kuchitapo kanthu.

 2. Umayi ndi umwana uyenera kuthandizidwa ndi kusamalidwa mwapadera.  Ana onse obadwa m'banja lozindikirika mwalamulo kapena losazindikirika adzatetezedwa umoyo wao mofanana.

Ndime 26

 1. Aliyense ali ndi ufulu kuphunzira.  Maphunziro akhale aulele makamaka ku pulaimale.  Maphunziro a pulaimale akhale oumiliza.  Maphunziro a zaluso ndi ena akhale opezeka ndipo maphunziro apamwamba a m'makoleji akhale opezeka kwa aliyense mofanana ndi nzeru zake.

 2. Maphunziro adzalinga kutukula umunthu, kulimbitsa ndi kulemekeza ufulu wa chibadwidwe wa munthu ndi ufulu wina ofunika.  Adzapititsa mtsogolo kumvetsa, kulemekeza maganizo a anthu ena, ubale wa maiko, mtundu, kapena magulu a zipembedzo, ndipo adzapititsa mtsogolo ntchito za bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations) posungitsa bata.

 3. Makolo ali ndi ufulu woyamba kusankha mtundu wa maphunziro amene akufunira ana awo.

Ndime 27

 1. Aliyense ali ndi ufulu kutenga nawo mbali pa zachikhalidwe cha anthu, kusangalala ndi zaluso ndiponso kugawana za sayansi ndi phindu lake.

 2. Aliyense ali ndi ufulu kutetezeredwa zomupindulira zonse zomwe zili zotsatira za ntchito ya sayansi, zolembalemba, kapena zaluso zina zomwe iye ndi mlembi wake.

Ndime 28

Aliyense ali oyenera kukhala bata ndi mtendere pa zomuthandiza pa moyo wake m'dziko lake ndi m'maiko mwina momwe ufulu wa chibadwidwe ndi ufulu wina walembedwa m'chikalata chino ungakwaniritsidwe kwathunthu.

Ndime 29

 1. Aliyense payekha ali ndi udindo kwa anthu ena amene akukhala nawo popeza ndi mwaiwo m'mene angathe kukwaniritsa  umunthu wake kwathunthu momasuka.
 2. Pokwaniritsa ufulu wake wachibadwidwe ndi ufulu wina, aliyense adzakhala ndi malire pokhapokha malamulo atero ndi cholinga chokwaniritsa kuzindikira ndi kulemekeza ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina wa ena ndiponso kukwaniritsa chilungamo, bata ndi kukhala bwino kwa anthu m'dziko lokomera anthu onse.
 3. Ufulu wa chibadwidwewu ndi ufulu  wina usagwiritsidwe ntchito mosagwirizana ndi zolinga ndi mfundo za bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations).

Ndime 30

Palibe chilichonse m'chikalata chino chomwe chingatanthauziridwe kuti dziko lililonse, gulu kapena munthu aliyense ali ndi ufulu kuchita chinthu ndi cholinga choononga ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina omwe wakhazikitsidwa m'chikalatachi.


  

 

 

 

MORE TRANSLATIONS UDHR

 

CHECHEWA ( Nyanja ) LANGUAGE

 

Chewa, also known as Nyanja, is a language of the Bantu language family. The gender prefix chi- is used for languages,[3] so the language is also known as Chichewa and Chinyanja (spelled Cinyanja in Zambia), and locally Nyasa in Mozambique.

Chewa is the national language of Malawi. It is also one of the seven official African languages of Zambia, where it is spoken mostly in the Eastern Province. It is also spoken in Mozambique, especially in the provinces of Tete and Niassa, as well as in Zimbabwe where, according to some estimates, it ranks as the third-most widely used local language, after Shona and Northern Ndebele. It was one of the 55 languages featured on the Voyager.

 

TOWN NYANJA

An urban variety of Nyanja, sometimes called Town Nyanja, is the lingua franca of the Zambian capital Lusaka and is widely spoken as a second language throughout Zambia. This is a distinctive Nyanja dialect with some features of Nsenga, although the language also incorporates large numbers of English-derived words, as well as showing influence from other Zambian languages such asBemba. Town Nyanja has no official status, and the presence of large numbers of loanwords and colloquial expressions has given rise to the misconception that it is an unstructured mixture of languages or a form of slang.

The fact that the standard Nyanja used in schools differs dramatically from the variety actually spoken in Lusaka has been identified as a barrier to the acquisition of literacy among Zambian children.[4] iSchool.zm, which develops online educational content in Zambian languages, has begun making 'Lusaka Nyanja' available as a separate language of instruction after finding that schoolchildren in Lusaka do not understand standard Nyanja.

HISTORY

Chinyanja has its origin in the Eastern Province of Zambia from the 15th century to the 18th century. The language remained dominant despite the breakup of the empire and theNguni invasions and was adopted by Christian missionaries at the beginning of the colonial period.

In Zambia, Chewa is spoken by other peoples like the Ngoni and the Kunda, so a more neutral name, Chinyanja "(language) of the lake" (referring to Lake Malawi), is used instead of Chewa.

The first grammar, A grammar of the Chinyanja language as spoken at Lake Nyasa with Chinyanja–English and English–Chinyanja vocabulary, was written by Alexander in 1880 and partial translations of the Bible were made at the end of 19th century. Further early grammars and vocabularies include A vocabulary of English–Chinyanja and Chinyanja–English: as spoken at Likoma, Lake Nyasa[5] and A grammar of Chinyanja, a language spoken in British Central Africa, on and near the shores of Lake Nyasa,[6] by George Henry (1891). The whole Bible was translated by William Percival Johnson and published as Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu in 1912.

A strong historical link of the Nyanja, Bemba and Yao people to the Shona Empire, who can point their earlier origins to Mashonaland, proves linguistically evident today. The ancient Shonas who temporarily dwelt in Malambo, a place in the DRC, eventually shifted into northern Zambia, and then south and east into the highlands of Malawi.

 

SAMPLE PHRASES

English Chewa (Malawi) Town Nyanja (Lusaka)
How are you? Muli bwanji? Muli bwanji?
I'm fine Ndili bwino Nili bwino / Nili mushe
Thank you Zikomo Zikomo
Yes Inde Ee
No Iyai Awe
What's your name? Dzina lanu ndani? Zina yanu ndimwe bandani?
My name is... Dzina langa ndine... Zina yanga ndine...
How many children do you have? Muli ndi ana angati? Muli na bana bangati?
I have two children Ndili ndi ana awiri Nili na bana babili
I want... Ndifuna... Nifuna...
Food Chakudya Chakudya
Water Madzi Manzi
How much is it? Ndi zingati? Ni zingati?
How much is it? Mukuchita bwanji?
See you tomorrow Tidzaonana mawa Tizaonana mailo

 

 

 

 

     
     
     

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Credits : wikipedia.org

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Credits : wikipedia.org | ohchr.org

 

 

 

UNITED NATIONS

OHCHR

GENERAL ASSEMBLY

SECURITY COUNCIL

UNICEF

UNESCO

HARVARD edX

WHO

UN CHARTER